Phungu wa nyumba ya malamulo ku Zomba Thondwe, a Roseby Gadama, wapereka ndalama zokwanira K1 million kwacha kuti ithandize ntchito zampingo.

A Gadama ndi mlendo olemekezeka pa mwambo wa mapemphero omwe akuchitika pansi pa utsogoleri wa m’mipingo wa Pastors Fraternal yaku Nasawa, Thondwe, Dzaone ndi Mayaka m’boma la Zomba. Iwo ati achita izi ngati njira imodzi yosangalalira kubadwa kwawo pa 1 October.

A Gadama akuti pa mwambowu, aperekanso galimoto la mtundu wa Ambulance, yomwe ati akuyembekezera kuti idzithandiza anthu m’dera la Zomba Thondwe. Iwo ati Ambulance imeneyi ndi mphatso ya anakubala.

Makwaya pafupifupi 20, kuphatikizapo Ndirande Anglican Voices atenga nawo gawo pa mwambo wa mapempherowu, womwe akuimbira ndi DJ Moda (Powered by DJ Moda). Pastor James Amidu a Coyem Church ndi Rev. David Kalumba a ku mpingo wa Powers on the Cross ndiwo alalikira pa mwambo wa mapempherowo.